Jeremiah 4:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta akuti “Paja anthu anga ndi opusa, Ine sandidziŵa. Ali ngati ana opulukira, osamvetsa chilichonse. Ali ndi luso pochita zoipa, koma kuchita zabwino sadziŵa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti anthu anga apusa, sandidziwa Ine; ali ana opulukira sazindikira; ali ochenjera kuchita choipa koma kuchita chabwino sakudziwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova akuti, “Anthu anga ndi zitsiru; iwo sandidziwa. Iwo ndi ana opanda nzeru; samvetsa chilichonse. Ali ndi luso lochita zoyipa, koma sadziwa kuchita zabwino.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti anthu anga apusa, sandidziwa Ine; ali ana opulukira sazindikira; ali ocenjera kucita coipa koma kucita cabwino sakudziwa.