Jeremiah 4:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidayang'ana, dziko la chonde linali litasanduka chipululu, mizinda yake yonse inali itasanduka mabwinja, chifukwa cha mkwiyo wa Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndinaona, ndipo taona, munda wazipatso unali chipululu, ndipo midzi yake yonse inapasuka pamaso pa Yehova, ndi pamaso pa mkwiyo wake woopsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinayangʼana, dziko lachonde linali litasanduka chipululu; mizinda yake yonse inali itasanduka bwinja pamaso pa Yehova, chifukwa cha mkwiyo wake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndinaona, ndipo taona, munda wazipatso unali cipululu, ndipo midzi yace yonse inapasuka pamaso pa Yehova, ndi pamaso pa mkwiyo wace woopsya.