Jeremiah 4:28 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chifukwa cha zimenezi dziko lonse lapansi lidzalira ndipo zakumwamba zidzachita mdima. Pakuti Ine ndalankhula, ndipo ndili ndi cholinga. Sindidafeŵe mtima, ndipo sindidzabwerera konse m'mbuyo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chimenecho dziko lidzalira maliro, ndipo kumwamba kudzada; chifukwa ndanena, ndatsimikiza mtima, sindinatembenuka, sindidzabwerera pamenepo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chifukwa chake dziko lapansi lidzalira ndipo thambo lidzachita mdima, pakuti ndayankhula ndipo sindidzafewa mtima, ndatsimikiza ndipo sindidzabwerera mʼmbuyo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cimeneco dziko lidzalira maliro, ndipo kumwamba kudzada; cifukwa ndanena, ndatsimikiza mtima, sindinatembenuka, sindidzabwerera pamenepo.