Jeremiah 4:31 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidamva kulira ngati kwa mkazi pa nthaŵi yake yochira, kubuula ngati kwa mkazi pa uchembere wake woyamba. Kumeneku kunali kulira kwa anthu a mu Ziyoni, ŵefuŵefu, atatambalitsa manja ao, akunena kuti, “Tsoka ife! Tikukomoka, moyo wathu waperekedwa kwa anthu otipha.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ndamva kubuula ngati kwa mkazi wobala, ndi msauko ngati wa mkazi wobala mwana wake woyamba, mau a mwana wamkazi wa Ziyoni wakupuma mosiyiza, wakutambasula manja ake, ndi kuti, Tsoka ine tsopano! Pakuti moyo wanga walefuka chifukwa cha ambanda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndikumva kulira ngati kwa mayi pa nthawi yake yobereka, kubuwula ngati kwa mayi amene akubereka mwana wake woyamba. Kuliraku ndi kwa anthu a mu Ziyoni, wefuwefu. Atambalitsa manja awo nʼkumati, “Kalanga ife! Tikukomoka. Moyo wathu waperekedwa kwa anthu otipha.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ndamva kubuula ngati kwa mkazi wobala, ndi msauko ngati wa mkazi wobala mwana wace woyamba, mau a mwana wamkazi wa Ziyoni wakupuma mosiyiza, wakutambasula manja ace, ndi kuti, Tsoka ine tsopano! pakuti moyo wanga walefuka cifukwa ca ambanda.