Jeremiah 4:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Monga momwe mkango umatulukira m'ngaka yake, momwemonso woononga maiko wanyamuka. Watuluka m'malo mwake kuti asakaze dziko lanu. Mizinda yanu idzakhala mabwinja popanda okhalamo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mkango wakwera kutuluka m'nkhalango mwake, ndipo woononga amitundu ali panjira, watuluka m'mbuto mwake kuti achititse dziko lako bwinja, kuti midzi yako ipasuke mulibenso wokhalamo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Monga mkango umatulukira mʼngaka yake momwemonso wowononga mayiko wanyamuka ndi kutuluka ku mbuto yake. Watero kuti awononge dziko lanu. Mizinda yanu idzakhala mabwinja popanda wokhalamo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mkango wakwera kuturuka m'nkhalango mwace, ndipo woononga amitundu ali panjira, waturuka m'mbuto mwace kuti acititse dziko lako bwinja, kuti midzi yako ipasuke mulibenso wokhalamo.