Jeremiah 4:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta akuti, “Pa tsiku limenelo mfumu ndi nduna zake, onse adzataya mtima. Ansembe adzaopsedwa, ndipo aneneri adzangoti kakasi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, ati Yehova, kuti mtima wa mfumu udzataika, ndi mitima ya akulu; ndipo ansembe adzazizwa, ndi aneneri adzadabwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Pa tsiku limenelo, mfumu ndi nduna zake adzataya mtima, ansembe adzachita mantha kwambiri, ndipo aneneri adzathedwa nzeru,” akutero Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, ati Yehova, kuti mtima wa mfumu udzatayika, ndi mitima ya akuru; ndipo ansembe adzazizwa, ndi aneneri adzadabwa.