Jeremiah 40:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ine nditsalira ku Mizipa kuti ndizikuimirirani kwa Ababiloni akamabwera. Koma inu mutenge zipatso zanu, vinyo wanu, mafuta anu, ndipo muzisunge ndithu. Muzikhala m'mizinda imene mwalandayo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ine, taonani, ndidzakhala pa Mizipa, ndiima pamaso pa Ababiloni, amene adzadza kwa ife; koma inu sonkhanitsani vinyo ndi zipatso zamalimwe ndi mafuta, muziike m'mbiya zanu, nimukhale m'midzi imene mwailanda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndidzakhala ku Mizipa kuti ndizikuyimirirani kwa Ababuloni amene azidzabwera kwa ife, koma inu muzikolola vinyo wanu, zipatso zanu, mafuta anu ndi kuzisunga mʼmitsuko yanu, nʼkumakhala mʼmizinda imene mwalandayo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ine, taonani, ndidzakhala pa Mizipa, ndiima pamaso pa Akasidi, amene adzadza kwa ife; koma inu, sonkhanitsani vinyo ndi zipatso zamalimwe ndi mafuta, muziike m'mbiya zanu, nimukhale m'midzi imene mwailanda.