Jeremiah 40:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nawonso Ayuda a ku Mowabu, ku Amoni ndi ku Edomu ndi a ku maiko ena, adamva kuti mfumu ya ku Babiloni idasiyako anthu ena ku Yuda, ndipo kuti idaŵaikira Gedaliya, mwana wa Ahikamu mdzukulu wa Safani, kuti akhale bwanamkubwa wao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chomwecho pamene Ayuda onse okhala m'Mowabu ndi mwa ana a Amoni, ndi m'Edomu, ndi amene anali m'maiko monse, anamva kuti mfumu ya ku Babiloni inasiya otsala a Yuda, ndi kuti inamuika Gedaliya mwana wa Ahikamu, mwana wa Safani wolamulira wao;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nawonso Ayuda onse a ku Mowabu, ku Amoni, ku Edomu ndi a ku mayiko ena onse anamva kuti mfumu ya ku Babuloni inasiyako anthu ena ku Yuda ndipo kuti inasankha Gedaliya mwana wa Ahikamu, mwana wa Safani, kukhala bwanamkubwa wawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Comweco pamene Ayuda onse okhala m'Moabu ndi mwa ana a Amoni, ndi m'Edomu, ndi amene anali m'maiko monse, anamva kuti mfumu ya ku Babulo inasiya otsala a Yuda, ndi kuti inamuika Gedaliya mwana wa Ahikamu, mwana wa Safani wolamulira wao;