Jeremiah 40:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adamufunsa kuti, “Kodi mukudziŵa kuti Baalisi mfumu ya Aamoni watuma Ismaele, mwana wa Netaniya kuti adzakupheni?” Koma Gedaliya mwana wa Ahikamu sadaŵakhulupirire.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nati kwa iye, Kodi mudziwa kuti Baalisi mfumu ya ana a Amoni watumiza Ismaele mwana wa Netaniya kuti akupheni inu? Koma Gedaliya mwana wa Ahikamu sanamvere iwo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndipo anamufunsa kuti, “Kodi sukudziwa kuti Baalisi mfumu ya Aamoni watuma Ismaeli mwana wa Netaniya kuti akuphe?” Koma Gedaliya mwana wa Ahikamu sanawankhulupirire.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nati kwa iye, Kodi mudziwa kuti Baalisi mfumu ya ana a Amoni watumiza Ismayeli mwana wa Netaniya kuti akupheni inu? Koma Gedaliya mwana wa Ahikamu sanamvera iwo.