Jeremiah 40:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Yohanani mwana wa Kareya, mwachinsinsi adauza Gedaliya kuti, “Loleni kuti ndikaphe Ismaele mwana wa Netaniyayu, ndipo wina aliyense sadzadziŵa. Nanga inu akuphereninji ndi kulola kuti Ayuda onse okuzunguliraniŵa amwazikane, ndipo otsala a ku Yuda adzaonongedwe?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yohanani mwana wa Kareya ananena kwa Gedaliya ku Mizipa m'tseri, kuti, Ndimuketu, ndikaphe Ismaele mwana wa Netaniya, anthu osadziwa; chifukwa chanji adzakuphani inu, kuti Ayuda onse amene anakusonkhanira inu amwazike, ndi otsala a Yuda aonongeke?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Yohanani mwana wa Kareya, mwamseri anawuza Gedaliya ku Mizipa kuti, “Loleni ndipite ndikaphe Ismaeli mwana wa Netaniya, ndipo palibe amene ati adziwe. Akuphereninji ndi kuchititsa Ayuda onse, amene akuzungulirani kuti abalalike ndi kuti otsala a ku Yuda awonongeke?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yohanani mwana wa Kareya ananena kwa Gedaliya m'tseri, kuti, Ndimuketu, ndikaphe Ismayeli mwana wa Netaniya, anthu osadziwa; cifukwa canji adzakuphani inu, kuti Ayuda onse amene anakusonkhanira inu amwazike, ndi otsala a Yuda aonongeke?