Jeremiah 40:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo zimenezi wazichitadi monga momwe adaanenera, chifukwa chakuti inu anthu mudachimwira Chauta, simudamumvere.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo Yehova wachitengera, ndi kuchita monga ananena, chifukwa mwachimwira Yehova, ndi kusamvera mau ake, chifukwa chake chinthu ichi chakufikirani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo tsopano Yehova wachitadi zimenezi monga mmene ananenera. Izi zonse zachitika chifukwa anthu inu munachimwira Yehova ndipo simunamumvere.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo Yehova wacitengera, ndi kucita monga ananena, cifukwa mwacimwira Yehova, ndi kusamvera mau ace, cifukwa cace cinthu ici cakufikirani.