Jeremiah 40:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma iwe Yeremiya, lero ndikukumasula maunyolo m'manjamu. Tiye ku Babiloni ngati ufuna, ndipo ndidzakusamala bwino. Koma ngati sufuna kupita, palibe kanthu. Dziko ndi lonseli monga ukuwonera, upite kumene uwona kuti nkoyenera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tsopano, taona, ndikumasula iwe lero maunyolo ali pa manja ako. Kukakukomera kudza nane ku Babiloni, idza, ndipo ndidzakusamalira bwino; koma kukakuipira kudza nane ku Babiloni, tsala; taona, dziko lonse lili pamaso pako; kulikonse ukuyesa kwabwino kapena koyenera kupitako, pita kumeneko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma tsopano taona, lero ndikukumasula unyolo umene unali mʼmanja mwako. Ngati ukufuna kupita nane ku Babuloni, tiye ndipo adzakusamala bwino. Koma ngati sukufuna kupita, ndiye usapite. Dziko ndi limeneli monga ukulioneramo. Uli ndi ufulu kupita kulikonse kumene ukufuna.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tsopano, taona, ndikumasula iwe lero maunyolo ali pa manja ako. Kukakukomera kudza nane ku Babulo, idza, ndipo ndidzakusamalira bwino; koma kukakuipira kudza nane ku Babulo, tsala; taona, dziko lonse liri pamaso pako; kuli konse ukuyesa kwabwino kapena koyenera kupitako, pita kumeneko.