Jeremiah 40:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngati supita, ubwerere kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu, mdzukulu wa Safani amene mfumu ya ku Babiloni idaamsankha kuti akhale bwanamkubwa wa mizinda ya ku Yuda. Ukakhale ndi iyeyo pakati pa anthu, kapena upite kulikonse kumene ufuna.” Tsono mtsogoleri wa nkhondo uja adampatsa chakudya, nampatsanso mphatso, ndipo adamuuza kuti, “Ai, pita bwino!”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsono asanabwerere iye anati, Bweratu kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu, mwana wa Safani, amene mfumu ya ku Babiloni inamyesa wolamulira midzi ya Yuda, nukhale naye pakati pa anthu; kapena pita kulikonse ukuyesa koyenera kupitako. Ndipo kapitao wa alonda anampatsa iye phoso ndi mtulo, namleka amuke.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yeremiya asanayankhe, Nebuzaradani anamuwuzanso kuti, “Ngati supita ndiye pita, ubwerere kwa Gedaliya, mwana wa Ahikamu, mdzukulu wa Safani, amene mfumu ya ku Babuloni inamusankha kuti akhale bwanamkubwa wa Yuda. Ukakhale naye pakati pa anthu, kapena upite kulikonse ukufuna.” Ndipo mtsogoleri uja anamupatsa Yeremiya chakudya ndi mphatso zina ndi kumulola kuti apite.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsono asanabwerere iye anati, Bweratu kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu, mwana wa Safani, amene mfumu ya ku Babulo inamyesa wolamulira midzi ya Yuda, nukhale naye pakati pa anthu; kapena pita kuli konse ukuyesa koyenera kupitako. Ndipo kapitao wa alonda anampatsa iye phoso ndi mtulo, namleka amuke.