Jeremiah 40:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Panali atsogoleri ena ankhondo amene sadadzipereke nao. Iwowo pamodzi ndi anthu ao adamva kuti mfumu ya ku Babiloni idaika Gedaliya, mwana wa Ahikamu, kuti akhale bwanamkubwa wa dzikolo, aziyang'anira anthu osauka kwambiri aja, amuna, akazi ndi ana, amene sadaŵatenge ukapolo kupita nawo ku Babiloni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene akulu onse a makamu amene anali m'minda, iwo ndi anthu ao, anamva kuti mfumu ya ku Babiloni adamuika Gedaliya mwana wa Ahikamu wolamulira dziko, nampatsira amuna, ndi akazi, ndi ana, ndi aumphawi a m'dzikomo, a iwo amene sanatengedwe ndende kunka nao ku Babiloni;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Panali atsogoleri ena a nkhondo ndi anthu awo amene sanadzipereke nawo. Iwowa anamva kuti mfumu ya ku Babuloni inasankha Gedaliya mwana wa Ahikamu kukhala bwanamkubwa wa dzikolo ndipo kuti yamuyika kukhala wolamulira amuna, akazi ndi ana amene anali osauka kwambiri mʼdzikomo, amene sanawagwire ukapolo kupita nawo ku Babuloni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene akuru onse a makamu amene anali m'minda, iwo ndi anthu ao, anamva kuti mfumu ya ku Babulo adamuika Gedaliya mwana wa Ahikamu wolamulira dziko, nampatsira amuna, ndi akazi, ndi ana, ndi aumphawi a m'dzikomo, a iwo amene sanatengedwa ndende kunka nao ku Babulo;