Jeremiah 40:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Onsewo, Gedaliya mwana wa Ahikamu, mdzukulu wa Safani, adaŵalonjeza molumbira kuti, “Musaope kuŵagwirira ntchito Ababiloniwo. Khalani m'dzikomu, muzimera mfumu ya ku Babiloni, ndipo zinthu zonse zidzakuyenderani bwino.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Gedaliya mwana wa Ahikamu mwana wa Safani anawalumbirira iwo ndi anthu ao, kuti, Musaope kuwatumikira Ababiloni; khalani m'dzikomu, mutumikire mfumu ya ku Babiloni, ndipo kudzakukomerani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Gedaliya mwana wa Ahikamu, mdzukulu wa Safani, anawalonjeza iwo pamodzi ndi anthuwo mwalumbiro. Ndipo anati, “Musaope kuwatumikira Ababuloni. Khalani mʼdziko muno, tumikirani mfumu ya ku Babuloni, ndipo zinthu zidzakuyenderani bwino.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Gedaliya mwana wa Ahikamu mwana wa Safani anawalumbirira iwo ndi anthu ao, kuti, Musaope kuwatumikira Akasidi; khalani m'dzikomu, mutumikire mfumu ya ku Babulo, ndipo kudzakukomerani.