Jeremiah 41:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa mwezi wachisanu ndi chiŵiri, Ismaele mwana wa Netaniya, mdzukulu wa Elisama, wa m'banja la mfumu, mmodzi mwa atsogoleri akuluakulu a mfumu, adafika ndi anthu khumi ku Mizipa kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu. Pamene ankadya naye kumeneko,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo panali mwezi wachisanu ndi chiwiri, Ismaele mwana wa Netaniya, mwana wa Elisama, wa mbeu ya mfumu, ndi kapitao wamkulu wa mfumu, ndi anthu khumi pamodzi ndi iye, anadza kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu ku Mizipa; pamenepo anadya pamodzi m'Mizipa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa mwezi wachisanu ndi chiwiri Ismaeli mwana wa Netaniya, mdzukulu wa Elisama amene anali wa banja laufumu ndiponso mmodzi wa atsogoleri a ankhondo a mfumu, anabwera ku Mizipa kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu ndi anthu khumi. Pamene ankadya naye kumeneko,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo panali mwezi wacisanu ndi ciwiri, Ismayeli mwana wa Netaniya, mwana wa Elisama, wa mbeu ya mfumu, ndi kapitao wamkuru wa mfumu, ndi anthu khumi pamodzi ndi iye, anadza kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu ku Mizipa; pamenepo anadya pamodzi m'Mizipa.