Jeremiah 41:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake Ismaele adaŵatenga ukapolo anthu onse amene adatsala ku Mizipa. Anthuwo ndi aŵa: ana aakazi a mfumu, ndi onse otsala ku Mizipa, amene Nebuzaradani mtsogoleri wa nkhondo adaŵapatsa Gedaliya mwana wa Ahikamu kuti akhale bwanamkubwa wao. Ndipo anthu ameneŵa adachoka nawo ndi cholinga choti akaloŵe nawo m'dziko la Aamoni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Ismaele anatenga ndende otsala onse a anthu okhala m'Mizipa, ana akazi a mfumu, ndi anthu onse amene anatsala m'Mizipa, amene Nebuzaradani kapitao wa alonda anapatsira Gedaliya mwana wa Ahikamu; Ismaele mwana wa Netaniya anawatenga ndende, napita kukaolokera kwa ana a Amoni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pambuyo pake Ismaeli anatenga ukapolo anthu ena onse amene anali ku Mizipa: ana aakazi a mfumu pamodzi ndi ena onse amene anatsalira kumeneko, amene Nebuzaradani mtsogoleri wa asilikali olonda mfumu anapatsa Gedaliya mwana wa Ahikamu kuti akhale bwanamkubwa wawo. Ismaeli mwana wa Netaliya anatenga ukapolo anthuwa ndi kuwoloka nawo kumapita ku dziko la Aamoni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Ismayeli anatenga ndende otsala onse a anthu okhala m'Mizipa, ana akazi a mfumu, ndi-anthu onse amene anatsala m'Mizipa, amene Nebuzaradani kapitao wa alonda anapatsira Gedaliya mwana wa Ahikamu; Ismayeli mwana wa Netaniya anawatenga ndende, napita kukaolokera kwa ana a Amoni.