Jeremiah 41:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu onse amene Ismaele adaaŵatenga ukapolo kuchoka nawo ku Mizipa, adabwerera napita kwa Yohanani mwana wa Kareya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anthu onse amene Ismaele anatenga ndende kuwachotsa m'Mizipa anatembenuka nabwera, nanka kwa Yohanani mwana wake wa Kareya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu onse amene Ismaeli anawagwira ukapolo ku Mizipa anabwerera ndi kupita kwa Yohanani mwana wa Kareya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anthu onse amene Ismayeli anatenga ndende kuwacotsa m'Mizipa anatembenuka nabwera, nanka kwa Yohanani mwana wace wa Kareya,