Jeremiah 41:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Yohanani mwana wa Kareya pamodzi ndi atsogoleri a magulu ankhondo, adatenga otsala a ku Mizipa amene Ismaele mwana wa Netaniya, adaaŵatenga ukapolo, atapha Gedaliya mwana wa Ahikamu. Amene adaŵatengawo anali ankhondo, akazi, ana ndi otumikira bwalo la mfumu, amene Yohanani adaabwera nawo kuchokera ku Gibiyoni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yohanani mwana wake wa Kareya ndi akazembe onse a makamu amene anali naye, anatenga anthu onse otsala a ku Mizipa, amene anawabweza kwa Ismaele mwana wake wa Netaniya atapha Gedaliya mwana wake wa Ahikamu, anthu a nkhondo, ndi akazi, ndi ana, ndi adindo, amene anawabwezanso ku Gibiyoni;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Yohanani mwana wa Kareya pamodzi ndi atsogoleri onse a ankhondo amene anali naye anatsogolera anthu onse otsala a ku Mizipa amene anawapulumutsa kwa Ismaeli mwana wa Netaniya atapha Gedaliya mwana wa Ahikamu. Anthu amenewa anali: asilikali, akazi, ana ndi amuna ofulidwa otumikira mfumu amene anawatenga ku Gibiyoni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yohanani mwana wace wa Kareya ndi akazembe onse a makamu amene anali naye, anatenga anthu onse otsala a ku Mizipa, amene anawabweza kwa Ismayeli mwana wace wa Netaniya atapha Gedaliya mwana wace wa Ahikamu, anthu a nkhondo, ndi akazi, ndi ana, ndi adindo, amene anawabwezanso ku Gibeoni;