Jeremiah 41:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ismaele, mwana wa Netaniya, pamodzi ndi anthu khumi aja, adadzambatuka napha Gedaliya mwana wa Ahikamu, mdzukulu wa Safani. Adamupha ndi malupanga ao munthu amene mfumu ya ku Babiloni idaamuika kuti akhale bwanamkubwa wa dziko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anauka Ismaele mwana wa Netaniya, ndi anthu khumi okhala naye, namkantha Gedaliya mwana wa Ahikamu mwana wa Safani ndi lupanga, namupha iye, amene mfumu ya ku Babiloni inamuika wolamulira dziko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ismaeli mwana wa Netaniya pamodzi ndi anthu khumi aja anayimirira ndi kupha ndi lupanga Gedaliya mwana wa Ahikamu, mdzukulu wa Safani. Choncho anapha munthu amene mfumu ya ku Babuloni inamusankha kukhala bwanamkubwa wa dzikolo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anauka Ismayeli mwana wa Netaniya, ndi anthu khumi okhala naye, namkantha Gedaliya mwana wa Ahikamu mwana wa Safani ndi lupanga, namupha iye, amene mfumu ya ku Babulo inamuika wolamulira dziko.