Jeremiah 41:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
kudafika anthu makumi asanu ndi atatu kuchokera ku Sekemu, ku Silo ndi ku Samariya. Ndevu zao adaameta, zovala zao zinali zong'ambikang'ambika, ndipo matupi ao anali otemekatemeka. Adatenga nsembe zaufa ndi lubani, kukapereka ku Nyumba ya Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
anadza anthu ochokera ku Sekemu, ndi ku Silo, ndi ku Samariya, anthu makamu asanu ndi atatu, atameta ndevu zao, atang'amba zovala zao, atadzitematema, anatenga nsembe zaufa ndi lubani m'manja mwao, kunka nazo kunyumba ya Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
kunafika anthu 80 ochekera ku Sekemu, Silo ndi Samariya, amene anali atameta ndevu zawo, atangʼamba zovala zawo ndi kudzichekacheka. Iwowa anatenga chopereka cha ufa ndi lubani kuti adzapereke ku Nyumba ya Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
anadza anthu ocokera ku Sekemu, ndi ku Silo, ndi ku Samariya, anthu makumi asanu ndi atatu, atameta ndebvu zao, atang'amba zobvala zao, atadzitematema, ana tenga nsembe zaufa ndi zonunkhira m'manja mwao, kunka nazo ku nyumba ya Yehova.