Jeremiah 41:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Ismaele, mwana wa Netaniya, adabwera akulira kuchokera ku Mizipa kudzakumana nawo. Atakumana nawo, adati, “Bwerani, mudzaonane ndi Gedaliya mwana wa Ahikamu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Ismaele mwana wa Netaniya anatuluka m'Mizipa kukakomana nao, alinkuyenda ndi kulira misozi; ndipo panali, pamene anakomana nao, anati kwa iwo, Idzani kwa Gedaliya mwana wake wa Ahikamu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ismaeli mwana wa Netaniya anachoka ku Mizipa akulira kupita kukakumana nawo. Atakumana nawo, iye anati, “Bwerani mudzaonane ndi Gedaliya mwana wa Ahikamu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Ismayeli mwana wa Netaniya anaturuka m'Mizipa kukakomana nao, alinkuyenda ndi kulira misozi; ndipo panali, pamene anakomana nao, anati kwa iwo, Idzani kwa Gedaliya mwana wace wa Ahikamu.