Jeremiah 41:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma pa gulu limenelo panali anthu khumi amene adaauza Ismaele kuti, “Ifeyo musatiphe, tili ndi tirigu, barele, mafuta, ndi uchi, zimene tidabisa m'minda.” Motero adaŵaleka osaŵaphera kumodzi ndi anzao aja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma mwa iwo anaoneka anthu khumi amene anati kwa Ismaele, Musatiphe ife; pakuti tili ndi chuma chobisika m'mudzi, cha tirigu, ndi cha barele, ndi cha mafuta, ndi cha uchi. Momwemo analeka, osawapha pakati pa abale ao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma anthu khumi a gululo anawuza Ismaeli kuti, “Musatiphe! Tili ndi tirigu ndi barele, mafuta ndi uchi, zimene tabisa mʼmunda.” Choncho anawasiya ndipo sanawaphere pamodzi ndi anzawo aja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma mwa iwo anaoneka anthu khumi amene anati kwa Ismayeli, Musatiphe ife; pakuti tiri ndi cuma cobisika m'mudzi, ca tirigu, ndi ca barele, ndi ca mafuta, ndi ca uci. Momwemo analeka, osawapha pakati pa abale ao.