Jeremiah 41:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chitsime chimene Ismaele adatayamo anthu amene adaŵapha aja chinali chitsime chachikulu chija chimene adaakumba ndi mfumu Asa, ataopsedwa ndi Basa mfumu ya ku Israele. Ismaele, mwana wa Netaniya adachidzaza ndi mitembo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo dzenje moponyamo Ismaele mitembo yonse ya anthu amene anawapha, chifukwa cha Gedaliya, ndilo analipanga mfumu Asa chifukwa cha kuopa Baasa mfumu ya Israele, lomwelo Ismaele mwana wa Netaniya analidzaza ndi ophedwawo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono chitsime chimene anaponyamo mitembo ya anthu amene anawaphawo pamodzi ndi mtembo wa Gedaliya chinali chimene mfumu Asa anachikumba poopsedwa ndi Baasa mfumu ya Israeli. Ismaeli mwana wa Netaliya anachidzaza ndi mitembo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo dzenje moponyamo Ismayeli mitembo yonse ya anthu amene anawapha, cifukwa ca Gedaliya, ndilo analipanga mfumu Asa cifukwa ca kuopa Raasa mfumu ya Israyeli, lomwelo Ismayeli mwana wa Netaniya analidzaza ndi ophedwawo.