Jeremiah 42:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
‘Ngati mukhala m'dziko lino, ndiye kuti mudzakhazikika, sindidzakuchotsani. Zoonadi, ndidzakukhazikitsani, osakuchotsani konse. Ndikumva chisoni chifukwa cha mazunzo amene ndidagwetsa pa inu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ngati mudzakhalabe m'dziko muno, ndidzamangitsa mudzi wanu, osakugumulani, ndidzakuokani inu, osakuzulani; pakuti ndagwidwa nacho chisoni choipa chimene ndakuchitirani inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ngati mukhala mʼdziko muno, ndiye kuti ndidzakukhazikitsani, osakuchotsani. Inde ndidzakudzalani osakuchotsani pakuti ndi kumva chisoni kwambiri chifukwa cha mavuto amene ndabweretsa pa inu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ngati mudzakhalabe m'dziko muno, ndidzamangitsa mudzi wanu, osakugumulani, ndidzakuokani inu, osakuzulani; pakuti ndagwidwa naco cisoni coipa cimene ndakucitirani inu.