Jeremiah 42:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Musaiwope mfumu ya ku Babiloni imene mukuiwopa tsopano. Musaiwope mfumuyo, chifukwa Ine ndili nanu, kuti ndikupulumutseni ndi kukuchotsani m'manja mwake, ndatero Ine Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Musaope mfumu ya ku Babiloni, amene mumuopa; musamuope, ati Yehova: pakuti Ine ndili ndi inu kukupulumutsani, ndi kukulanditsani m'dzanja lake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Musayiope mfumu ya ku Babuloni, imene mukuyiopa tsopano. Musachite nayo mantha, akutero Yehova, pakuti Ine ndili nanu ndipo ndidzakupulumutsani ndi kukulanditsani mʼmanja mwake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Musaope mfumu ya ku Babulo, amene mumuopa; musamuope, ati Yehova: pakuti Ine ndiri ndi inu kukupulumutsani, ndi kukulanditsani m'dzanja lace.