Jeremiah 42:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mukatero, inu otsala a ku Yuda, imvani mau aŵa a Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele. Akunena kuti, ‘Mukatsimikiza za kupita ku Ejipitozi, nkupitadi kukakhala kumeneko,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
chifukwa chake mumve mau a Yehova, Otsala inu a Yuda, atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, Ngati mulozetsa nkhope zanu kuti mulowe m'Ejipito, kukakhala m'menemo;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono, inu otsala a ku Yuda, imvani mawu a Yehova. Iye akuti, ngati mutsimikiza zopita ku Igupto, nʼkupitadi kukakhala kumeneko,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
cifukwa cace mumve mau a Yehova, Otsala inu a Yuda, atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli, Ngati mulozetsa nkhope zanu kuti mulowe m'Aigupto, kukakhala m'menemo;