Jeremiah 42:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu onse amene akutsimikiza za kupitadi ku Ejipito, ndi kukakhala kumeneko, adzafa ndi nkhondo, njala ndiponso mliri. Palibe ndi mmodzi yemwe amene adzatsale kapena kupulumuka ku zoopsa zimene ndidzaŵagwetsere.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kudzatero ndi anthu onse akulozetsa nkhope zao anke ku Ejipito kuti akhale kumeneko; adzafa ndi lupanga, ndi njala, ndi chaola; ndipo wa iwo sadzatsala kapena kupulumuka ku choipa chimene ndidzatengera pa iwo ngakhale mmodzi yense.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kunena zoona, onse amene atsimikiza zopita ku Igupto kuti akakhale kumeneko adzafa ndi nkhondo njala ndi mliri. Palibe ndi mmodzi yemwe amene adzapulumuke kapena kuthawa mavuto amene ndidzawagwetsera.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kudzatero ndi anthu onse akulozetsa nkhope zao anke ku Aigupto kuti akhale kumeneko; adzafa ndi lupanga, ndi njala, ndi caola; ndipo wa iwo sadzatsala kapena kupulumuka ku coipa cimene ndidzatengera pa iwo ngakhale mmodzi yense.