Jeremiah 42:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akunenanso kuti, ‘Monga momwe anthu okhala ku Yerusalemu ndidaŵakwiyira mwaukali, momwemonso ndidzakukwiyirani inuyo mukadzapita ku Ejipito. Mudzasanduka chinthu chonyansa ndi chochititsa mantha, chomachiseka ndi chonyozeka. Malo ano simudzaŵaonanso.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Monga mkwiyo wanga ndi ukali wanga wathiridwa kwa okhala m'Yerusalemu, momwemo ukali wanga udzathiridwa pa inu, pamene mudzalowa m'Ejipito; ndipo mudzakhala chitukwano, ndi chizizwitso, ndi chitemberero, ndi chitonzo; ndipo simudzaonananso malo ano.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti, ‘Momwe ndinawakwiyira mwaukali anthu okhala mu Yerusalemu, koteronso ndidzakukwiyirani mukapita ku Igupto. Mudzasanduka chinthu chotembereredwa ndi chochititsa mantha, choseketsa ndi chonyozeka. Malo ano simudzawaonanso.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Monga mkwiyo wanga ndi ukali wanga wathiridwa kwa okhala m'Yerusalemu, momwemo ukali wanga udzathiridwa pa inu, pamene mudzalowa m'Aigupto; ndipo mudzakhala citukwano, ndi cizizwitso, ndi citemberero, ndi citonzo; ndipo simudzaonanso malo ano.