Jeremiah 42:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ife tabwera ndi dandaulo lathu. Chonde, mutipempherere kwa Chauta, Mulungu wanu, ife amene tatsala oŵerengeka. Tangotsalatu ochepa chabe pa anthu ambiri, monga mukutiwoneramu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nati kwa Yeremiya mneneri, Chipembedzero chathu chigwe pamaso panu, nimutipempherere ife kwa Ambuye Mulungu wanu, chifukwa cha otsala onsewa; pakuti tatsala ife owerengeka m'malo mwa ambiri, monga maso anu ationa ife;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
kwa mneneri Yeremiya ndipo anamuwuza kuti, “Chonde imvani dandawulo lathu ndipo mutipempherere anthu otsalafe kwa Yehova Mulungu wanu. Pakuti monga tsopano mukuona, ngakhale kuti kale tinalipo ambiri, koma tsopano ochepa okha ndiye amene atsala.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nati kwa Yeremiya mneneri, Cipembedzero cathu cigwe pamaso panu, nimutipempherere ife kwa Ambuye Mulungu wanu, cifukwa ca otsala onsewa; pakuti tatsala ife owerengeka m'malo mwa ambiri, monga maso anu ationa ife;