Jeremiah 42:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Paja mudaandituma kwa Chauta Mulungu wanu ndi kunena kuti, ‘Mutipempherere kwa Chauta Mulungu wathu, ndipo mutiwuze chilichonse chimene Chauta Mulungu wathu ati anene, ife tidzazichita.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti mwanyenga m'miyoyo yanu; pakuti mwandituma ine kwa Yehova Mulungu wanu, ndi kuti, Mutipempherere ife kwa Yehova Mulungu wathu; ndipo monga mwa zonse Yehova Mulungu wathu adzanena, momwemo mutifotokozere ife; ndipo tidzachita.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
kuti munalakwitsa kwambiri. Inu munandituma kwa Yehova Mulungu wanu nʼkumati ‘Mukatipempherere kwa Yehova Mulungu wathu, nʼkudzatiwuza chimene afuna kuti tichite, ndipo ife tidzachita.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti mwanyenga m'miyoyo yanu; pakuti mwandituma ine kwa Yehova Mulungu wanu, ndi kuti, Mutipempherere ife kwa Yehova Mulungu wathu; ndipo monga mwa zonse Yehova Mulungu wathu adzanena, momwemo mutifotokozere ife; ndipo tidzacita.