Jeremiah 42:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwowo adauza Yeremiya kuti, “Chauta akhale mboni yoona ndi yokhulupirika yodzatitsutsa ngati sitichita zimene Chauta Mulungu wanu wakutumani kuti mudzatiwuze.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo iwo anati kwa Yeremiya, Yehova akhale mboni yoona ndi yokhulupirika pakati pa ife, ngati sitichita monga mwa mau onse Yehova Mulungu wanu adzakutumizani nao kwa ife.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo iwo anawuza Yeremiya kuti, “Yehova akhale mboni yoona ndi yokhulupirika yodzatitsutsa ife ngati sitichita mogwirizana ndi chilichonse chimene Yehova Mulungu adzakutumani kuti mutiwuze.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo iwo anati kwa Yeremiya, Yehova akhale mboni yoona ndi yokhulupirika pakati pa ife, ngati siticita monga mwa mau onse Yehova Mulungu wanu adzakutumizani nao kwa ife.