Jeremiah 42:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kaya nzabwino, kaya zoipa, tidzamvera ndithu mau a Chauta Mulungu wathu, amene takutumani kuti mukampemphe kanthu m'dzina lathu. Tidzamvera Chauta Mulungu wathu, kuti zinthu zitiyendere bwino.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ngakhale ali abwino, ngakhale ali oipa, ife tidzamvera mau a Yehova Mulungu wathu, kwa Iye amene tikutumizani inu; kuti kutikomere, pomvera mau a Yehova Mulungu wathu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kaya ndi zotikomera kapena zosatikomera, ife tidzamvera Yehova Mulungu wathu, amene takutumaniko. Tidzamvera Yehova Mulungu wathu kuti zinthu zidzatiyendere bwino.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ngakhale ali abwino, ngakhale ali oipa, ife tidzamvera mau a Yehova Mulungu wathu, kwa Iye amene tikutumizani inu; kuti kutikomere, pomvera mau a Yehova Mulungu wathu.