Jeremiah 43:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono uŵauze kuti Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akunena kuti, ‘Ndidzaitana mtumiki wanga Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni. Iyeyo adzaika mpando wake pa miyala imene ndaibisa apoyo. Ndipo adzafunyulula hema lake laufumu pa miyalayo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi kuti kwa iwo, Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Taonani Ine ndidzatuma ndidzatenga Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, mtumiki wanga, ndi kuika mpando wake wachifumu pa miyalayi ndaiyala; ndipo iye adzaivundikira ndi hema wachifumu wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo uwawuze kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Ndidzayitana mtumiki wanga Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni, ndipo adzakhazika mpando wake waufumu pa miyala imene ndayikwirira apayi. Iye adzafunyulula tenti yake yaufumu pa miyala imeneyi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi kuti kwa iwo, Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Taonani Ine ndidzatuma ndidzatenga Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo, mtumiki wanga, ndi kuika mpando wace wacifumu pa miyalayi ndaiyala; ndipo iye adzaibvundikira ndi hema wacifumu wace.