Jeremiah 43:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adzabwera kudzaononga Ejipito, adzatumiza mliri pa anthu oyenera kufa ndi mliri, adzatenga ukapolo anthu oyenera kutengedwa ukapolo, ndipo adzaŵapha ndi lupanga oyenera kuphedwa ndi lupanga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iye adzafika, nadzakantha dziko la Ejipito; nadzapereka kuimfa iwo a kuimfa, ndi kundende iwo a kundende, ndi kulupanga iwo a kulupanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye adzabwera kudzathira nkhondo Igupto. Iwo oyenera kufa ndi mliri adzafa ndi mliri, iwo oyenera kutengedwa ukapolo adzatengedwa ukapolo, ndipo iwo oyenera kufa ndi lupanga adzafa ndi lupanga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iye adzafika, nadzakantha dziko la Aigupto; nadzapereka kuimfa iwo a kuimfa, ndi kundende iwo a kundende, ndi kulupanga iwo a kulupanga.