Jeremiah 43:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adzasonkha moto m'nyumba za milungu ya ku Ejipito. Adzatentha nyumbazo, ndipo milunguyo adzaitenga kupita nayo ku ukapolo. Adzayeretsa dziko la Ejipito monga momwe mbusa amamangira chovala chake m'chiuno, momwemonso ndimo adzaŵachitire Aejiptio ndipo adzachoka ku Ejipito osaona vuto lililonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndidzayatsa moto m'nyumba za milungu ya Ejipito; ndipo adzazitentha, nadzaitenga ndende; ndipo adzadzifunda ndi dziko la Ejipito, monga mbusa avala chovala chake; nadzatuluka m'menemo ndi mtendere.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Adzayatsa moto mʼnyumba zopembedzera milungu ya Igupto. Adzayeretsa dziko la Igupto monga momwe mʼbusa amayeretsera chovala chake pochotsamo nsabwe. Pambuyo pake adzachoka mʼdziko la Igupto mwa mtendere.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndidzayatsa moto m'nyumba za milungu ya Aigupto; ndipo adzazitentha, nadzaitenga ndende; ndipo adzadzipfunda ndi dziko la Aigupto, monga mbusa abvala cobvala cace; nadzaturuka m'menemo ndi mtendere.