Jeremiah 43:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adzaphwanya zipilala zachipembedzo za ku nyumba yopembedzeramo mulungu wa dzuŵa ku Ejipito. Ndipo adzatentha nyumba za milungu ya ku Ejipito.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo adzathyola mizati ya zoimiritsa za Kachisi wa dzuwa, ali m'dziko la Ejipito; ndi nyumba za milungu ya Aejipito adzazitentha ndi moto.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ku Iguptoko adzagwetsa zipilala zachipembedzo za ku nyumba yopembedzera mulungu wa dzuwa. Adzatentha ndi moto nyumba za milungu ya ku Igupto.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo adzatyola mizati ya zoimiritsa za kacisi wa dzuwa, ali m'dziko la Aigupto; ndi nyumba za milungu ya Aigupto adzazitentha ndi moto.