Jeremiah 43:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Azariya mwana wa Hesaya, Yohanani mwana wa Kareya, ndiponso anthu onse achipongwe, adauza Yeremiya kuti, “Iwe ukunama. Chauta Mulungu wathu sadakutume kudzanena kuti, ‘Musapite ku Ejipito kukakhala kumeneko.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pamenepo ananena Azariya mwana wake wa Hosaya, ndi Yohanani mwana wake wa Kareya, ndi anthu onse odzikuza, nati kwa Yeremiya, Unena zonama; Yehova Mulungu wathu sanakutumize iwe kudzanena, Musalowe m'Ejipito kukhala m'menemo;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Azariya mwana wa Hosayia ndi Yohanani mwana wa Kareya pamodzi ndi anthu onse odzikuza anawuza Yeremiya kuti, “Ukunama iwe! Yehova Mulungu wathu sanakutume kuti unene kuti, ‘Musapite ku Igupto kukakhala kumeneko.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pamenepo ananena Azariya mwana wace wa Hosaya, ndi Yohanani mwana wace wa Kareya, ndi anthu onse odzikuza, nati kwa Yeremiya, Unena zonama; Yehova Mulungu wathu sanakutumiza iwe kudzanena, Musalowe m'Aigupto kukhala m'menemo;