Jeremiah 43:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Baruki mwana wa Neriya ndiye wakukakamiza kuti utiletse, ndipo kuti tigwe m'manja mwa Ababiloni, kuti atiphe kapena kutitenga ukapolo kupita ku Babiloni.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma Baruki mwana wake wa Neriya atichichizira inu, mutipereke m'dzanja la Ababiloni, kuti atiphe ife, atitengere ife am'nsinga ku Babiloni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ndi Baruki mwana wa Neriya amene akukulimbikitsa kuti utiletse zopita ku Igupto ndi kuti mʼmalo mwake tidzipereke mʼmanja mwa Ababuloni, kuti iwo atiphe kapena kutitenga ukapolo ku Babuloni.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma Baruki mwana wace wa Neriya aticicizira inu, mutipereke m'dzanja la Akasidi, kuti atiphe ife, atitengere ife am'nsinga ku Babulo.