Jeremiah 43:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho Yohanani mwana wa Kareya, pamodzi ndi atsogoleri a ankhondo, adatenga anthu onse otsala a ku Yuda amene adabwerera kuchokera ku maiko kumene adaabalalikira kuti akakhale ku Yuda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Yohanani mwana wake wa Kareya, ndi akazembe onse a nkhondo, anatenga otsala onse a Yuda, amene anabwera kumitundu yonse kumene anaingitsidwirako kuti akhale m'dziko la Yuda;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼmalo mwake, Yohanani mwana wa Kareya ndi atsogoleri onse a ankhondo anatenga anthu onse otsala a ku Yuda amene anabwera kudzakhala mʼdziko la Yuda kuchokera ku mayiko onse kumene anabalakirako.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Yohanani mwana wace wa Kareya, ndi akazembe onse: a nkhondo, anatenga otsala onse a Yuda, amene anabwera ku mitundu yonse kumene anaingitsidwirako kuti akhale m'dziko la Yuda;