Jeremiah 43:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthuwo anali aŵa: amuna, akazi ndi ana, kuphatikizapo ana aakazi a mfumu, ndiponso anthu onse amene Nebuzaradani, mtsogoleri wa ankhondo adaaŵasiya kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu, mdzukulu wa Safani. Adatenganso mneneri Yeremiya ndi Baruki mwana wa Neriya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi amuna, ndi akazi, ndi ana, ndi ana akazi a mfumu, ndi anthu onse amene Nebuzaradani kapitao wa alonda anasiya ndi Gedaliya mwana wake wa Ahikamu, mwana wake wa Safani, ndi Yeremiya mneneri, ndi Baruki mwana wake wa Neriya;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼgulu la anthu otengedwalo munali amuna onse, akazi ndi ana, ana aakazi a mfumu, ndiponso anthu amene Nebuzaradani mtsogoleri wa asilikali olonda mfumu anawasiya kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu, mdzukulu wa Safani pamodzinso ndi mneneri Yeremiya ndi Baruki mwana wa Neriya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi amuna, ndi akazi, ndi ana, ndi ana akazi a mfumu, ndi anthu onse amene Nebuzaradani kapitao Wa alonda anasiya ndi Gedaliya mwana wace wa Ahikamu, mwana wace wa Safani, ndi Yeremiya mneneri, ndi Baruki mwana wace wa Neriya;