Jeremiah 43:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Tenga miyala ina yaikulu, uikwirire m'dothi pa chiwundo cha poloŵera ku nyumba yaufumu ya Farao ku Tapanesi. Ayuda akuwone ukuchita zimenezo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tenga miyala yaikulu m'dzanja lako, nuiyale ndi dothi pakati pa njerwa, za pa khomo la nyumba ya Farao m'Tapanesi pamaso pa anthu a Yuda;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Tenga miyala inayi yayikulu ndipo uyikwirire mʼdothi pa chiwundo cha polowera ku nyumba yaufumu ya Farao ku Tapanesi. Uchite zimenezi Ayuda onse akuona.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tenga miyala yaikuru m'dzanja lako, nuiyale ndi dothi pakati pa njerwa, za pa khomo la nyumba ya Farao m'Tapanesi pamaso pa anthu a Yuda;