Jeremiah 44:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nawu uthenga umene Yeremiya adalandira wonena za Ayuda amene ankakhala ku dziko la Ejipito ku Migidoli, ku Tapanesi, ku Memfisi ndi ku dziko la Patirosi:
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mau amene anadza kwa Yeremiya onena za Ayuda onse amene anakhala m'dziko la Ejipito, okhala pa Migidoli, ndi pa Tapanesi, ndi pa Nofi, ndi m'dziko la Patirosi, akuti,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Uthenga umene Yeremiya analandira wonena za Ayuda onse amene ankakhala ku Igupto, ku mizinda ya Migidoli, Tapanesi ndi Mefisi, ndiponso ku Patirosi ndi uwu:
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mau amene anadza kwa Yeremiya onena za Ayuda onse amene anakhala m'dziko la Aigupto, okhala pa Migidoli, ndi pa Tapanesi, ndi pa Nofi, ndi m'dziko la Patirosi, akuti,