Jeremiah 44:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzatenga anthu otsala a ku Yuda amene adatsimikiza zopita ku Ejipito kukakhala kumeneko, onsewo adzatheratu. Adzaphedwa m'dziko la Ejipito, ena adzafa pa nkhondo, ena adzafa ndi njala. Ang'onoang'ono ndi akuluakulu omwe adzafadi pa nkhondo kapena kufa ndi njala. Ndipo adzasanduka chinthu chonyansa ndi chochititsa mantha, chinthu chomachiseka ndi chonyozeka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzatenga otsala a Yuda, amene analozetsa nkhope zao alowe m'dziko la Ejipito akhale m'menemo, ndipo adzathedwa onse; m'dziko la Ejipito adzagwa, adzathedwa ndi lupanga ndi njala; adzafa kuyambira wamng'ono mpaka wamkulu, ndi lupanga ndi njala; ndipo adzakhala chitukwano, ndi chizizwitso, ndi chitemberero, ndi chitonzo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzatenga anthu otsala a ku Yuda amene atsimikiza zopita ku Igupto ndi kukakhala kumeneko. Onse adzathera ku Igupto. Adzaphedwa ndi lupanga kapena kufa ndi njala. Kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu, adzaphedwa ndi lupanga kapena kufa ndi njala. Adzasanduka chinthu chotembereredwa ndi chochititsa mantha, chinthu choseketsa ndi chonyozeka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzatengaotsala a Yuda, amene analozetsa nkhope zao alowe m'dziko la Aigupto akhale m'menemo, ndipo adzathedwa onse; m'dziko la Aigupto adzagwa, adzathedwa ndi lupanga ndi njala; adzafa kuyambira wamng'ono mpaka wamkuru, ndi lupanga ndi njala; ndipo adzakhala citukwano, ndi cizizwitso, ndi citemberero, ndi citonzo.