Jeremiah 44:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzalanga Ayuda okhala ku Ejipito monga momwe ndidalangira a ku Yerusalemu. Ndidzaŵalanga ndi nkhondo, njala ndi mliri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzalanga iwo okhala m'dziko la Ejipito, monga ndinalanga Yerusalemu, ndi lupanga, ndi njala, ndi chaola;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzalanga Ayuda okhala ku Igupto ndi lupanga, njala ndi mliri, ngati mmene ndinalangira anthu a ku Yerusalemu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzalanga iwo okhala m'dziko la Aigupto, monga ndinalanga Yerusalemu, ndi lupanga, ndi njala, ndi caola;