Jeremiah 44:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero mwa anthu otsala ku Yuda, amene adapita nakakhala ku Ejipito, palibe amene adzapulumuke, kapena kukhala moyo, kapena kubwerera ndi kukakhalanso ku Yuda komwe ankalakalaka. Palibe amene adzabwerere, kungopatula ena othaŵa nkhondo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kuti otsala a Yuda, amene ananka kudziko la Ejipito kukhala m'menemo, asapulumuke asatsale ndi mmodzi yense, kuti abwere kudziko la Yuda, kumene afuna kubwera kuti akhale m'menemo; pakuti adzabwera koma adzapulumuka ndiwo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Motero mwa anthu amene anapita ku Igupto palibe ndi mmodzi yemwe adzapulumuke, kapena kukhala ndi moyo, kapena kubwerera ku Yuda. Palibe amene adzabwerere kupatula othawa nkhondo.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kuti otsala a Yuda, amene ananka ku dziko la Aigupto kukhala m'menemo, asapulumuke asatsale ndi mmodzi yense, kuti abwere ku dziko la Yuda, kumene afuna kubwera kuti akhale m'menemo; pakuti adzabwera koma adzapulumuka ndiwo.