Jeremiah 44:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono amuna onse amene adadziŵa kuti akazi ao ankafukizira lubani milungu ina, ndiponso akazi onse amene anali pamenepo, anthu ochuluka ndithu, kudzanso anthu onse amene ankakhala ku Patirosi m'dziko la Ejipito, adayankha Yeremiya kuti,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo amuna onse amene anadziwa kuti akazi ao anafukizira milungu ina, ndi akazi onse omwe anaimirirapo, msonkhano waukulu, anthu onse okhala m'dziko la Ejipito, m'Patirosi, anamyankha Yeremiya, kuti,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono amuna onse amene anadziwa kuti akazi awo ankafukiza lubani kwa milungu ina, ndiponso akazi onse amene anali pamenepo, gulu lalikulu la anthu, pamodzi ndi anthu onse amene amakhala ku Patirosi mʼdziko la Igupto, anati kwa Yeremiya,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo amuna onse amene anadziwa kuti akazi ao anafukizira milungu yina, ndi akazi onse omwe anaimirirapo, msonkhano waukuru, anthu onse okhala m'dziko la Aigupto, m'Patirosi, anamyankha Yeremiya, kuti,