Jeremiah 44:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma tidzachitadi zonse zimene tidalumbira. Tidzaifukizira ndithu lubani mfumukazi yakumwamba ndi kuiperekera nsembe zazakumwa, monga tinkachitira ifeyo ndi makolo athu, mafumu athu ndi akalonga athu, m'mizinda ya ku Yuda ndi m'miseu ya mu Yerusalemu. Nthaŵi imeneyo tinali ndi chakudya chambiri, ndipo tinkakhuta, osapeza zovuta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma tidzachita ndithu mau onse anatuluka m'kamwa mwathu, kufukizira mfumu yaikazi ya kumwamba, ndi kumthirira iye nsembe zothira, monga momwe tikachitira ife, ndi atate athu, ndi mafumu athu ndi akulu athu, m'midzi ya Yuda, ndi m'miseu ya Yerusalemu, pakuti pamenepo tinali ndi chakudya chokwanira, tinakhala bwino, sitinaona choipa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma tidzachitadi chilichonse chimene tinanena kuti tidzachita: Tidzafukiza lubani kwa mfumukazi yakumwamba ndipo tidzayipatsa nsembe yachakumwa ngati mmene tinkachitira ifeyo ndi makolo athu, mafumu athu ndi akuluakulu mʼmizinda ya ku Yuda ndi mʼmisewu ya mu Yerusalemu. Nthawi imeneyo ife tinali ndi chakudya chochuluka ndipo tinali pabwino, sitimapeza mavuto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma tidzacita ndithu mau onse anaturuka m'kamwa mwathu, kufukizira mfumu yaikazi ya kumwamba, ndi kumthirira iye nsembe zothira, monga momwe tikacitira ife, ndi atate athu, ndi mafumu athu ndi akuru athu, m'midzi ya Yuda, ndi m'miseu ya Yerusalemu, pakuti pamenepo tinali ndi cakudya cokwanira, tinakhala bwino, sitinaona coipa.