Jeremiah 44:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma kuchokera nthaŵi imene tidaleka kuifukizira lubani mfumukazi yakumwamba, ndi kumaiperekera nsembe zazakumwa, takhala tikusoŵa zonse, ndipo taonongeka ndi nkhondo ndi njala.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma chilekere ife kufukizira mfumu yaikazi ya kumwamba, ndi kumthirira iye nsembe zothira, tasowa zonse, tathedwa ndi lupanga ndi chaola.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma kuchokera nthawi imene tinasiya kufukiza lubani ndi kupereka chopereka cha chakumwa kwa mfumukazi yakumwamba, ifeyo takhala tikusowa zinthu ndipo takhala tikuphedwa ndi lupanga ndi kufa ndi njala.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma cilekere ife kufukizira mfumu yaikazi ya kumwamba, ndi kumthirira iye nsembe zothira, tasowa zonse, tathedwa ndi lupanga ndi caola.