Jeremiah 44:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Akaziwo adapitirira ponena kuti, “Pamene tinkaifukizira lubani mfumukazi yakumwamba ndi kumaiperekera nsembe zazakumwa, kodi suja amuna athu ankavomereza m'mene tinkapangira mfumukaziyo makeke abwino olembapo chithunzi chake, ndiponso m'mene tinkaiperekera nsembe zazakumwa?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene tinafukizira mfumu yaikazi ya kumwamba, ndi kumthirira nsembe zothira, kodi tinamuumbira iye mikate yakumpembedzera, ndi kumthirira nsembe zothira, opanda amuna athu?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Akazi anawonjezera kunena kuti, “Pamene tinkafukiza lubani kwa mfumukazi yakumwamba ndi kuyipatsa chopereka cha chakumwa, kodi suja amuna athu ankavomereza mmene timayipangira mfumukazi yakumwambayo makeke abwino olembapo chinthunzi chake ndi kuyipatsa chopereka cha chakumwa?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene tinafukizira mfumu yaikazi ya kumwamba, ndi kumthirira nsembe zothira, kodi tinamuumbira iye mikate yakumpembedzera, ndi kumthirira nsembe zothira, opanda amuna athu?